Job 3

Mawu a Yobu

1Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. 2Ndipo Yobu anati:

3“Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe
ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
4Tsiku limenelo lisanduke mdima;
Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso;
kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
5Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli;
mtambo uphimbe tsikuli;
mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
6Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani;
usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka,
kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
7Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino;
kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
8Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo,
iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
9Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima;
tsikulo liyembekezere kucha pachabe
ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
10Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga
ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.

11“Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa
ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
12Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo
ndi mawere woti andiyamwitsepo?
13Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere;
ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
14pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi,
amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
15pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide,
amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
16Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale,
ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
17Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto,
ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
18A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere;
sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
19Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko,
ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.

20“Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto,
ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
21kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera,
amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
22amene amakondwa ndi kusangalala
akamalowa mʼmanda?
23Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu
amene njira yake yabisika,
amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
24Mʼmalo moti ndidye, ndimalira,
ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
25Chimene ndinkachiopa chandigwera;
chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
26Ndilibe mtendere kapena bata,
ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
Copyright information for NyaCCL